Kumvera mwa khungu?

“Tisamongoti poti a Papa ndi a Papa!

Tchalitchi chimatiphunzitsa kumvera mopanda kukayika: ‘Mtima womvera ndi chifuniro ndi khalidwe lolemeka akulu. Komabe pauphunzitsi wokhudza zakumvera mchikhristu payenera kukhala umboni wokewanira kuti ndi uphunzitsi wowona wochokera kwa a Papa, angakhalenso pomwe a Papawo

sakukamba mfundo zomwe mzosatsutsika chifuka cha mphamvu zomwe a Papa alinazo mu u udindo wawo ngati Papa;izi zikutznthauza kuti, pomwe a Papa akupereka phunziro anthu aenera kumadzionera okha kutidi ndi uphunzitsa wowona, ndipo anthu adzitha kutsatiza mwaulemu ndipo zizikhala zotsogozedwa ndi mphatso za luntha zomwe a Papa amalandira kuchokera kwa Mzimu Woyera.”
Lumen Gentium, § 25c.

“Nkhaniyi siipherezera pano!

Kulemekeza akulu ndi kumvera kwenikweni sikusowa kuti tiphe chikumbumtima, tisakhale ndi nthumanzi kapenenso kuti tisatsate zomwe tikudziwa mosapeneka kuti ndi zoona!

Nsonkhano wa Khansolo yachiwiri ku Vatikani umatiphunzitsa kuti:: ‘Akulu wolamulira adzichita nthumanzi potsatira malamulo ndiponso pogwira ntchito ya utsogoleri.atiphunzitsanso kuti atsogeleri adzigwiritsa ntchito molinganga ndi luntha ndi maganizo awo, ndiponso pogwiritsa ntchto mphatso zawo zachilengedwe ndi zi zomwe amalandira kuchokera kwa Mzimu Woyera.’

Ndi m’njira yokhayi, Khansoliyi idatero, momwe kumvera sikuchotsa ulemu wa umunthu wa anthu woganiza bwino. Kumvera mu m’njira imeyi kumakuza kukhwima maganizo ndi ufulu zomwe ndi mphatso zoyenerera ana a Mulungu.
Perfectae Caritatis § 14.

“Kodi mwaiwala uphunzitsi wapamwa wa a Iginasiyo Woyera wa kuLoyola?

Iye adati, kumvera mwakhungu, kumatisandutsa ngati mtengo wakufa womwe ena amasandutsa ndodo yoyendera.

Kumvera moona kumatipangitsa kuti tivomereze kuti kanthumkoyera, ngakhale pa nthawi yomwe tikukawona kuti mkakuda!”

“Mzoonadi a Iginasio adatero. Komano awa anali mawu okuluwika. Sitingakainso, kodi sipaja iwowa ankafuna kuti atumiki a mchipani cha Majeziwiti, chipani chomwe iwo adaambitsa, kuti akhale anthu a mzeru, olungama ndipo a luntha pa zounikira maganizo osiyanasiyana?

Tanthauzo labwino la kumvera ndilo lomwe limalemekeza maganizo abwino aanthu potsatira maufulu awo ndipo mopanda mantha. Awa ndiye matanthauzo ena abwino a kumvera:

  • ‘Kumvera ndi kumvetsera chifuniro cha Mulungu mu mtima mwathu: ndi kutsatiza mopanda mantha nthumanzi ndi chikumbumtima chathu, monga chisomo chikutiunukira, ndiponso pomvetsera maganizo ma limana athu… choncho kumvera Khristu, kumvera a Bishopu athu, kumvera Mulungu — zonsezi magwero ake ali mu khumbo lofunitsitsa kukhala mwana wa Mulungu nchifanizo cha ufulu wa Mulungu.’
    Barbara Schmitz akuti
  • ‘Kumvera moona sikutanthauza kukhala okonzeka kutumikira ena nthawi zonse basi, komanso kuima patokha mosaopa pa maganizo ofunika ndi kuunikira bwino maganizo wena opanda pake amene angasokoneze maganizo athu angwiro’.
    Joan Chittister

Mchifukwa chiyani tikutsutsana ndi uphunzitsi wa mpingo wa mtsankhoMafunso apafupipafupiZina?
kusintha kwa chikalidwemfundombirikumvera kwenikweninthumanzi ya chikhulupiriro
ufulu wokhala mayi?uphunzitsi wosatsutsika?kudalilika?kumvera?kederera?
Kodi ‘maufulu’ a aKatolika mtchalitchi ndi ati?
Muli ndi mafunso? __Maganizo ena? __Ndemanga?